YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 26

26
1Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:
2Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo; 3makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima. 4Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene anakhala chiyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse; 5#Mac. 22.3andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu. 6#Gen. 22.18; Deut. 18.1; Yes. 9.6; Mac. 13.32; 23.6Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu analichita kwa makolo athu; 7kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda. 8Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa? 9#Mac. 8.3; 9.14; Agal. 1.13; 1Tim. 1.13Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo. 10#Mac. 8.3; 9.14; Agal. 1.13; 1Tim. 1.13Chimenenso ndinachita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo. 11#Mac. 22.19Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumidzi yakunja.
12 # Mac. 9.3 M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe aakulu, 13dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza. 14Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira. 15Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda. 16#Mac. 22.15Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe; 17#Mac. 22.21ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo, 18#Yes. 35.5; Luk. 1.77; Yoh. 8.12; Aef. 1.11; Akol. 1.13kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine. 19Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba; 20#Mac. 9.20, 22, 29komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima. 21#Mac. 21.30-31Chifukwa cha izi Ayuda anandigwira m'Kachisi, nayesa kundipha. 22#Mac. 24.14Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika; 23#Luk. 24.26, 46; 1Ako. 15.20kuti Khristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.
24 # Yoh. 10.20 Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau akulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala. 25Koma Paulo anati, Ndilibe misala, Fesito womvekatu; koma nditulutsa mau a choonadi ndi odziletsa. 26Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitika m'tseri. 27Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa kuti muwakhulupirira. 28Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera mkhristu. 29#1Ako. 7.7Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.
30Ndipo ananyamuka mfumu, ndi kazembe, ndi Berenise, ndi iwo akukhala nao; 31#Mac. 23.9ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzake, nanena, Munthu uyu sanachita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga. 32#Mac. 25.11Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwa Kaisara.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in