MACHITIDWE A ATUMWI 25
25
Paulo pa bwalo la milandu la Fesito. Anena akatulukira kwa Kaisara
1Pamenepo Fesito m'mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya. 2#Mac. 25.15Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira, 3#Mac. 23.12, 15nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira. 4Pamenepo Fesito anayankha, kuti Paulo asungike ku Kesareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa. 5#Mac. 18.14Chifukwa chake, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.
6Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo. 7#Luk. 23.2, 10; Mac. 24.5, 13Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanakhoza kuzitsimikiza; 8#Mac. 6.13; 24.12; 28.17koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwa kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara. 9#Mac. 25.20Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi? 10Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino. 11#Mac. 25.25Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara. 12#Mac. 26.32; 28.19Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.
Paulo adzinenera kwa Agripa
13Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Berenise anafika ku Kesareya, nalankhula Fesito. 14#Mac. 24.27Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Fesito anafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felikisi, 15#Mac. 25.2-6amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake. 16Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho. 17Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwa, koma m'mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo. 18Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamtchulira konse chifukwa cha zoipa zonga ndinazilingirira ine; 19#Mac. 18.15koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo. 20Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi. 21Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara. 22Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.
23M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao akulu, ndi amuna omveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo. 24#Mac. 22.22Ndipo Fesito anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo. 25#Mac. 23.9, 29; 25.11-12Koma ndinapeza ine kuti sanachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako. 26Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera. 27Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 25: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi