YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 24

24
Felikisi amva mlandu wa Paulo
1 # Mac. 23.2, 30, 35 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo. 2Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa, 3tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu. 4Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu. 5#Luk. 23.2Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene; 6#Mac. 21.28amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira.#24.6 Mabuku ena akale amaonjezerapo mau awa: Ndipo tidafuna kumuweruza potsata Malamulo athu. 7 Koma Lisiasi, mkulu wa asilikali, adadzamtsomphola kumanja kwathu mwankhondo, 8 kenaka nkulamula kuti omneneza adzaonekere kwa inu. 8Ndipo kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi. 9Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.
10Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera; 11popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira; 12ndipo sanandipeza m'Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda. 13Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano. 14#Aro. 1.9Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri; 15#Tit. 2.13; Yoh. 5.28-29ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama. 16#Mac. 23.1M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu. 17#Mac. 20.16; Aro. 15.25Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka; 18#Mac. 21.26-28popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; 19#Mac. 23.30koma panali Ayuda ena a ku Asiya, ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine. 20Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akulu, 21#Mac. 23.6koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.
22Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu. 23#Mac. 27.3Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.
24Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu. 25Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe. 26#Eks. 23.8Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye. 27#Mac. 12.3Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in