MACHITIDWE A ATUMWI 23
23
1 #
1Ako. 4.4; 2Tim. 1.3 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.
2 #
Yoh. 18.22
Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake. 3#Lev. 19.35; Yoh. 7.51Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo? 4Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu? 5#Eks. 22.28; Mac. 24.17Ndipo Paulo anati, Sindinadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako. 6#Mac. 15.21Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa. 7Ndipo pamene adatero, kunakhala chilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana. 8#Mat. 22.23Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri. 9#Mac. 25.25Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye? 10Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.
11 #
Mac. 18.9; 27.23-24 Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.
Ayuda apangana chiwembu cha kupha Paulo. Apulumukira ku Kesareya
12Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo; 13ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi anali oposa makumi anai. 14Amenewo anadza kwa ansembe aakulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo. 15Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye. 16Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo. 17Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye. 18Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu. 19Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera? 20#Mac. 23.12Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye. 21Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu. 22Pamenepo ndipo kapitao wamkulu anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi. 23Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku; 24ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.
25Ndipo analembera kalata wakuti: 26Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni. 27#Mac. 21.31-33Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma. 28#Mac. 22.30Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye ku bwalo la akulu ao. 29#Mac. 18.15Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga. 30#Mac. 23.20; 24.8Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.
31Pamenepo ndipo asilikali, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri. 32Koma m'mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga; 33iwowo, m'mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye. 34#Mac. 21.39Ndipo m'mene adawerenga anafunsa achokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Silisiya, 35#Mac. 24.1, 10anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba ya milandu ya Herode.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 23: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi