MACHITIDWE A ATUMWI 22
22
Paulo achita chodzikanira chake kwa anthu
1Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.
2Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati: 3#Mac. 5.34; 21.20, 39Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero; 4#Mac. 8.3ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi. 5#Mac. 9.2Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe. 6#Mac. 9.3-8; 26.12-18Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba. 7Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? 8Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda. 9Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamva mau akulankhula nane. 10Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite. 11Ndipo popeza sindinapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko. 12#Mac. 9.17Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako, 13anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya. 14#Mac. 9.15Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake. 15#Mac. 23.11Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva. 16#Mac. 9.18Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake. 17#Mac. 9.26Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kachisi, ndinachita ngati kukomoka, 18ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine. 19Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu; 20#Mac. 7.58ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye. 21#Mac. 13.46-47Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.
22 #
Mac. 21.36
Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo. 23Ndipo pakufuula iwo, ndi kutaya zovala zao, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga, 24kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho. 25#Mac. 16.37Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka? 26Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma. 27Ndipo kapitao wamkuluyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde. 28Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma. 29Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.
Paulo pa bwalo la akulu
30Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 22: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi