MACHITIDWE A ATUMWI 21
21
Paulo atabwera ku Yerusalemu amgwira m'Kachisi
1Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m'mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara; 2ndipo m'mene tinapeza ngalawa yakuoloka kunka ku Fenisiya, tinalowamo, ndi kupita nayo. 3Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake. 4#Mac. 21.12Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu. 5#Mac. 20.36Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera, 6ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.
7Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wochokera ku Tiro, tinafika ku Ptolemaisi; ndipo m'mene tidalonjera abale, tinakhala nao tsiku limodzi. 8#Mac. 6.5Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye. 9Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera. 10#Mac. 11.28Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lake Agabu. 11#Mac. 20.23; 21.33Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu. 12Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu. 13#Mat. 16.21-23; 20.24Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu. 14#Mat. 6.10Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.
15Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu. 16Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.
17Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera. 18#Mac. 15.13Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo. 19#Mac. 15.4, 12Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake. 20#Mac. 22.3; Aro. 10.2Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo; 21ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo. 22Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika. 23Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda; 24#Mac. 18.18amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo. 25#Mac. 15.20, 29Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama. 26#Num. 6.13; Mac. 24.18Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
27 #
Mac. 24.18
Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira, 28#Mac. 24.5-6nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao m'Kachisi, nadetsa malo ano oyera. 29Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi. 30#Mac. 26.21Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m'Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa. 31Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti m'Yerusalemu monse muli piringupiringu. 32#Mac. 23.27Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo. 33#Mac. 21.11Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani? 34Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga. 35Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo; 36#Luk. 23.18pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.
37Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki? 38Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu? 39#Mac. 22.3Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Silisiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu. 40Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 21: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi