YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 20

20
Paulo apitanso ku Masedoniya, ndi Grisi, ndi Asiya
1Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya. 2Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi. 3#Mac. 23.12Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya. 4Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo. 5Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Troasi. 6Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.
7 # 1Ako. 16.2 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku. 8Ndipo munali nyali zambiri m'chipinda chapamwamba m'mene tinasonkhanamo. 9Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa. 10#1Maf. 17.21Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo. 11Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kucha, anachokapo. 12Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.
13Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha. 14Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene. 15Ndipo m'mene tidachokerapo, m'mawa mwake tinafika pandunji pa Kiyo; ndi m'mawa mwake tinangokocheza ku Samo, ndi m'mawa mwake tinafika ku Mileto. 16#Mac. 24.17Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.
Mau a Paulo kwa akulu a ku Efeso
17Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo. 18Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse, 19#Mac. 20.3wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda; 20#Mac. 20.27kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu, 21#Mrk. 1.15ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 22Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko; 23#Mac. 9.16; 21.4, 11koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira. 24#Mac. 21.13; Agal. 1.1Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu. 25#Mac. 20.38Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga. 26#Mac. 18.6Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse. 27#Mac. 20.20Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu. 28#Aef. 1.7, 14; 1Pet. 5.2Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha. 29#Mat. 7.15Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; 30ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate. 31#Mac. 19.10Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi. 32#Aef. 1.14, 18Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa. 33#1Sam. 12.3; 1Ako. 9.12Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense. 34#Mac. 18.3Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine. 35#1Sam. 12.3; 1Ako. 9.12M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.
36 # Mac. 21.5 Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse. 37Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona, 38#Mat. 6.10nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in