YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 19

19
Ulendo wachitatu wa Paulo. Demetrio autsa phokoso
1 # 1Ako. 1.12; 3.5-6 Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena; 2#Yoh. 7.39; Mac. 18.25ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa. 3#Mac. 18.25Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane. 4#Mat. 3.11Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu. 5#Mac. 8.16Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. 6#Mac. 8.17Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera. 7Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.
8 # Mac. 17.2 Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu. 9Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano. 10#Mac. 20.31Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki. 11#Mrk. 16.20Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo; 12#Mac. 5.15kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka. 13Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. 14Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene anachita ichi. 15Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani? 16Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa. 17#Mac. 5.5, 11Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika. 18Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao. 19Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu. 20#Mac. 12.24Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.
21 # Mac. 23.11; Aro. 15.24-28 Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma. 22Pamene anatuma ku Masedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi m'Asiya. 23Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo. 24#Mac. 16.16, 19Pakuti munthu wina dzina lake Demetrio wosula siliva, amene anapanga tiakachisi tasiliva, ta Aritemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri; 25amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza chuma chathu. 26#Mas. 115.4; Yes. 44.10-20Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja: 27ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza. 28Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, nafuula, nati, Wamkulu ndi Aritemi wa ku Efeso. 29Ndipo m'mudzi monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo. 30Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, ophunzira ake sanamloleza. 31Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ake, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye kubwalo lakusewera. 32Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa chifukwa chake cha kusonkhana. 33Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo. 34Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akufuula monga maora awiri, Wamkulu ndi Aritemi wa Aefeso. 35Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi? 36Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu kaliuma. 37Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano. 38Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane. 39Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa. 40Pakutinso palipo potiopsa kuti adzatineneza za chipolowe chalero; popeza palibe chifukwa cha kufotokozera za chipiringu chimene. 41Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in