MACHITIDWE A ATUMWI 14
14
Uthenga Wabwino ulalikidwa ku Ikonio, Listara, ndi Deribe
1Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira. 2Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu. 3#Mrk. 16.20Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao. 4Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi. 5#2Tim. 3.11Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala, 6#Mat. 10.23iwo anamva, nathawira kumidzi ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo: 7kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.
8 #
Mac. 3.2
Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayenda nthawi zonse. 9#Mat. 9.28-29Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo, 10#Mat. 9.28-29anati ndi mau akulu, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda. 11#Mac. 28.6Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu. 12Ndipo anamutcha Barnabasi, Zeusi; ndi Paulo, Heremesi, chifukwa anali wotsogola kunena. 13Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu. 14Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu, 15#Yak. 5.17nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo: 16#Mac. 17.30m'mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao. 17#Mac. 17.27; Aro. 1.20Koma sanadzisiyira Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero. 18Pakunena izo, anavutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 #
Mac. 13.35; 2Ako. 11.25 Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa. 20Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe. 21#Mat. 28.19Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya, 22#Mat. 16.24; Mac. 13.43nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri. 23Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo. 24Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfiliya. 25Ndipo atalankhula mau m'Perga, anatsikira ku Ataliya; 26#Mac. 13.1, 3komweko anachoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo. 27#Mac. 15.3-4, 12Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro. 28Ndipo anakhala pamenepo ndi ophunzira nthawi yaikulu.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 14: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi