MACHITIDWE A ATUMWI 15
15
Ku Yerusalemu atumwi ndi akulu aweruza za mdulidwe ndi Malamulo a Mose
1 #
Lev. 12.3; Agal. 2.12 Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka. 2#Agal. 2.1Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo. 3#Mac. 14.27Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse. 4#Mac. 14.27Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao. 5#Mac. 15.1Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.
6Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo. 7#Mac. 10.20Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire. 8#Mac. 10.44Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife; 9#Aro. 10.11-12ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro. 10#Mat. 23.4Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife? 11#Aef. 2.8; Tit. 2.11Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe.
12 #
Mac. 14.27
Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu. 13Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine: 14#Mac. 15.7Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. 15Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa,
16 #
Amo. 9.11-12
Zikatha izo ndidzabwera,
ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa;
ndidzamanganso zopasuka zake,
ndipo ndidzachiimikanso:
17Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,
ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo,
18ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo
chiyambire dziko lapansi.
19Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu, 20#Eks. 20.3, 23; Lev. 3.17; 1Ako. 6.9, 18koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi. 21#Mac. 13.15, 27Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'midzi yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m'masunagoge masabata onse.
22Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo: 23Atumwi ndi abale akulu kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikulankhulani: 24#Mac. 15.1Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira; 25chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo, 26#Mac. 13.50; 14.19anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu. 27Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo. 28Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; 29#Mac. 15.20kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.
30Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo. 31Pamene anawerenga, anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake. 32Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa. 33Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.#15.33 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 34 Koma kudamkomera Silasi kukhalabe kumeneko. 35#Mac. 13.1Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe m'Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.
Paulo ndi Barnabasi alekana
36 #
Mac. 13—14
Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerenso, tizonde abale m'midzi yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao. 37#Mac. 12.12, 25; 13.5, 13; 2Tim. 4.11Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko 38Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito. 39Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m'ngalawa, nanka ku Kipro.
Ulendo wachiwiri wa Paulo
40 #
Mac. 14.26
Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye. 41#Mac. 16.5Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi