MACHITIDWE A ATUMWI 13
13
Ulendo woyamba wa Paulo. Mpingo wa ku Antiokeya utuma Paulo ndi Barnabasi amuke kwa amitundu. Alalikira pa Kipro. Elimasi watsenga
1 #
Mac. 11.27
Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo. 2#Num. 8.14; Mac. 9.15; Aro. 1.1; Aef. 3.7-8Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.
3Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.
4Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m'ngalawa ku Kipro. 5#Mac. 13.46Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao. 6#Mac. 8.9Ndipo m'mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu; 7ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu. 8#Eks. 7.11Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire. 9#Mac. 4.8Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye, 10nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye? 11#1Sam. 5.6Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja. 12Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.
Mau a Paulo m'sunagoge wa Antiokeya wa m'Pisidiya
13 #
Mac. 15.37-38
Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu. 14#Mac. 17.1-2Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi. 15#Luk. 4.16-17Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani. 16Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani. 17#Deut. 7.6-8Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo. 18#Eks. 16.35Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu. 19#Yos. 14.1-2Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m'Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu; 20#Ower. 2.16ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo. 21#1Sam. 8.5Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai. 22#1Sam. 16.13Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. 23#Yes. 11.1Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu; 24#Mat. 3.1-2Yohane atalalikiratu, asanafike Iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israele. 25#Mat. 3.11Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake. 26Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi. 27#Mac. 13.14-15Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa. 28#Mrk. 15.13-14Ndipo ngakhale sanapeza chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe. 29#Luk. 18.31Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda. 30#Mat. 28.6Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa; 31#1Ako. 15.5-7ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu. 32#Gen. 12.3Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo; 33kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala. 34#Yes. 55.3Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide. 35#Mas. 16.10Chifukwa anenanso m'Salimo lina, Simudzapereka Woyera wanu aone chivundi. 36Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi; 37koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona chivundi. 38#Luk. 24.47Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo; 39#Aro. 3.28ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose. 40Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:
41 #
Hab. 1.5
Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;
kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu,
ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.
42Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo. 43#Mac. 14.22Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m'chisomo cha Mulungu.
44Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu. 45Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano. 46#Mat. 10.6; 21.43; Mac. 28.28Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu. 47#Yes. 42.6Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti,
Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu,
kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.
48Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha. 49Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse. 50#2Tim. 3.11Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao. 51#Mat. 10.14Koma iwo, m'mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio. 52#Mat. 5.12Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi