YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 12

12
Herode azunza Mpingo; amupha Yakobo, naponya Petro kundende. Petro apulumuka m'ndende. Imfa ya Herode
1Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Mpingo kuwachitira zoipa. 2#Mat. 4.2Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane. 3Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa. 4#Yoh. 21.18Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska. 5Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza. 6Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende. 7#Mac. 5.19Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake. 8Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine. 9Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya. 10#Mac. 16.26Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumudzi; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera. 11#Mas. 34.7, 22Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda. 12#Mac. 4.23; 12.5Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza kunyumba ya Maria amake wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera. 13Ndipo m'mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda. 14Ndipo pozindikira mau ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo. 15Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wake. 16Koma Petro anakhala chigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa. 17Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina. 18Koma kutacha, panali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti. 19Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.
20Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu. 21Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo. 22Ndipo anthu osonkhanidwawo anafuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai. 23#1Sam. 25.38; Mas. 115.1Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.
24 # Akol. 1.6 Koma mau a Mulungu anakula, nachulukitsa. 25#Mac. 12.12; 13.5, 13 Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in