MACHITIDWE A ATUMWI 11
11
Petro adziwerengera pamaso pa Mpingo kuti anabatiza Korneliyo
1Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu. 2#Agal. 2.12Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo akumdulidwe anatsutsana naye, 3#Mac. 10.28nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao. 4Koma Petro anayamba kuwafotokozera chilongosolere, nanena, 5#Mac. 10.9-32Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine; 6chimenecho ndidachipenyetsetsa ndinachilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zilombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga. 7Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye. 8Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. 9Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba. 10Ndipo ichi chinachitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba. 11Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya. 12Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo; 13ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro; 14amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse. 15#Mac. 2.4Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja. 16#Mac. 1.5Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera. 17#Mac. 10.47Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu? 18#Aro. 10.12-13Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.
Uthenga Wabwino ulalikidwa kwa amitundu a ku Antiokeya
19 #
Mac. 8.1
Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha. 20#Mac. 9.29Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. 21#Mac. 2.47; 9.35Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupirira unatembenukira kwa Ambuye. 22#Mac. 9.27Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya; 23ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye; 24#Mac. 6.5; 11.21chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye. 25#Mac. 9.30Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo; 26ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
27 #
Mac. 13.1; 15.32 Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya. 28#Mac. 21.10Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio. 29#1Ako. 16.1Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya; 30#Mac. 12.25ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi