YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 10

10
Kenturiyo Kornelio
1Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya, 2#Mac. 10.22ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka. 3#Mac. 10.30Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio. 4Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu. 5Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, aitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro; 6#Mac. 9.43acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja. 7Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka; 8ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa.
9 # Mac. 11.5 Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya; 10koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; 11#Mac. 7.56ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi chotengera chilinkutsika, chonga ngati chinsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinai, ndi kutsikira padziko pansi; 12m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga. 13Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye. 14#Lev. 20.25Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa. 15#Aro. 14.17, 20Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba. 16Ndipo chinachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chinatengedwa kunka kumwamba.
17Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata, 18ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wotchedwanso Petro, acherezedwako. 19#Mac. 11.12Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe. 20#Mac. 11.12Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine. 21Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; chifukwa chake mwadzera nchiyani? 22#Mac. 22.12Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu. 23#Mac. 11.12Pamenepo anawalowetsa nawachereza.
Ndipo m'mawa mwake ananyamuka natuluka nao, ndi ena a abale a ku Yopa anamperekeza iye. 24Ndipo m'mawa mwake analowa m'Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni. 25Ndipo panali pakulowa Petro, Kornelio anakomana naye, nagwa pa mapazi ake, namlambira. 26#Mac. 14.14-15Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu. 27Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana; 28#Yoh. 4.9; 18.28; Mac. 15.8-9ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa; 29chifukwa chakenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji? 30Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira, 31#Aheb. 6.10nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu. 32Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja. 33Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.
34 # Deut. 10.17; Aro. 2.11; Aef. 6.9 Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; 35#Aro. 2.13, 27; Agal. 3.28koma m'mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye. 36#Aro. 10.12; 1Ako. 15.27; Aef. 2.14, 16-17Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse) 37#Luk. 4.14mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira; 38#Luk. 4.18; Yoh. 3.2; Mac. 4.27za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye. 39#Mac. 2.32Ndipo ife ndife mboni za zonse adazichita m'dziko la Ayuda ndi m'Yerusalemu; amenenso anamupha, nampachika pamtengo. 40#Mac. 2.24Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti aonetsedwe, 41#Luk. 24.30, 43si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa. 42#Mat. 28.19-20; Yoh. 5.22, 27Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa. 43#Yes. 28.16; Yes. 53.11; Zek. 13.1Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.
44 # Mac. 8.15-17 Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. 45#Mac. 10.23; Agal. 3.14Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. 46Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, 47#Aro. 10.12Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? 48#Mac. 2.38Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in