YouVersion Logo
Search Icon

3 YOHANE 1

1
1 # 2Yoh. 1 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi.
2Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera. 3#2Yoh. 4Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi.
Za kuchereza abale ndi alendo
4 # 1Ako. 4.15 Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'choonadi.
5Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe; 6amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino: 7#1Ako. 9.12, 15pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. 8Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.
Za Diotrefe ndi Demetrio
9Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife. 10Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo. 11#Yes. 1.16-17; 1Yoh. 2.29Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu. 12#Yoh. 21.24; 1Tim. 3.7Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.
13Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni; 14koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana. 15Mtendere ukhale nawe. Akupereka moni abwenzi. Upereke moni kwa abwenzi ndi kutchula maina ao.

Currently Selected:

3 YOHANE 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in