YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 7

7
Mulungu salola Davide ammangire nyumba
1Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira, 2#Eks. 26.1; 2Sam. 5.11mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga. 3#1Maf. 8.17-18Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani muchite chonse chili mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu. 4Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti, 5#1Maf. 5.3Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine? 6#Eks. 40.18Pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba. 7M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israele kodi ndinanena ndi fuko limodzi la Aisraele, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisraele, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza? 8#1Sam. 16.11-12Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele. 9#Gen. 12.2; 1Sam. 18.14Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali pa dziko lapansi. 10#Yer. 24.6; 1Maf. 11.38Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja, 11monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. 12#1Maf. 8.20Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 13#1Maf. 5.5Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse. 14#Mas. 89.26-27, 30-33; Aheb. 1.5Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu; 15#1Sam. 15.23, 28koma chifundo changa sichidzamchokera iye, monga ndinachichotsera Saulo amene ndinamchotsa pamaso pako. 16#Luk. 1.33; Yoh. 12.34Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse. 17Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.
18 # Gen. 32.10 Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano? 19#2Sam. 7.12-13Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu! 20#Mas. 139.1-4Ndipo Davide adzaonjezanso kunenanso ndi Inu? Pakuti mudziwa mnyamata wanu, Yehova Mulungu. 21Chifukwa cha mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munachita ukulu wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu. 22#Mas. 48.1; Yes. 45.5Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu. 23#Deut. 4.7, 32, 34Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao? 24#Deut. 14.2Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisraele, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao. 25Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yake, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimuchite monga munalankhula. 26Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu. 27Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu. 28#Yoh. 17.17Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munalonjezana ndi mnyamata wanu kumchitira chabwino ichi, 29chifukwa chake tsono chikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu chikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munachinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.

Currently Selected:

2 SAMUELE 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in