2 SAMUELE 8
8
Davide agonjetsa amitundu ena
1 #
1Mbi. 18.1
Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti. 2#2Sam. 8.6, 14Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. 3#Gen. 15.18; 1Mbi. 18.3Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate. 4#Yos. 11.6, 9Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi. 5Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri. 6#2Sam. 8.14Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako. 7Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu. 8Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu. 9Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere, 10Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa. 11#1Maf. 7.51Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa; 12za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba. 13Ndipo Davide anamveketsa dzina lake pamene anabwera uko adakantha Aaramu m'Chigwa cha Mchere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu. 14#1Sam. 8.6Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
15Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse. 16Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri, 17ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi. 18Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.
Currently Selected:
2 SAMUELE 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi