2 SAMUELE 6
6
Atenga likasa la Mulungu kunyumba ya Abinadabu
1Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israele, anthu zikwi makumi atatu. 2#Eks. 25.22Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi. 3#1Sam. 6.7Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo. 4#1Sam. 7.1Potuluka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu ili pachitunda, Ahiyo anatsogolera likasalo. 5Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje. 6#Num. 4.15Ndipo pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lake, nachirikiza likasa la Mulungu; chifukwa ng'ombe zikadapulumuka. 7#1Sam. 6.19Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu. 8Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino. 9#Mas. 119.120; Luk. 5.8-9Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine? 10Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti. 11#1Mbi. 13.13-14Ndipo likasa la Yehova linakhala m'nyumba ya Obededomu Mgiti miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa Obededomu ndi banja lake lonse.
Akwera nalo likasalo kuliika ku Yerusalemu
12 #
1Mbi. 15.25
Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumudzi wa Davide, ali ndi chimwemwe. 13Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china. 14#Mas. 30.11Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta. 15Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga. 16Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake. 17#1Maf. 8.5, 62-63; 1Mbi. 15.1Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. 18#1Maf. 8.14, 55Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu. 19#1Mbi. 16.3Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake. 20Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi! 21Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova. 22Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa. 23Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake.
Currently Selected:
2 SAMUELE 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi
Free Reading Plans and Devotionals related to 2 SAMUELE 6

Reading With the People of God #10 Kingdom

Naked And Unafraid

Bible Stories: Old Testament Season 2
