YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 5

5
Mafuko onse avomereza Davide mfumu yao
1 # Gen. 29.14 Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu. 2#1Sam. 18.13, 16; Mas. 78.71Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele. 3#2Maf. 11.17Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.
4Davide anali ndi zaka makumi atatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi anai. 5#2Sam. 2.11Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.
Davide alanda Yerusalemu
6 # Yos. 15.63 Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno. 7Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mudzi wa Davide. 8Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo. 9#1Maf. 9.15Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe. 10Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.
11 # 1Maf. 5.2 Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba. 12Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele.
13Ndipo Davide anadzitengera akazi aang'ono ena ndi akazi a ulemu ena a ku Yerusalemu, atafikako kuchokera ku Hebroni; ndipo anambadwira Davide ana aamuna ndi aakazi. 14Maina a iwo anambadwira m'Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, 15ndi Ibara ndi Elisuwa, ndi Nefegi ndi Yafiya; 16ndi Elisama ndi Eliyada ndi Elifeleti.
Davide akantha Afilisti
17 # 1Mbi. 14.8 Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja. 18Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu. 19Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako. 20Ndipo Davide anafika ku Baala-Perazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu. 21#Deut. 7.5, 25Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ake nawachotsa.
22Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu. 23Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku. 24#Ower. 4.14; 2Maf. 7.6Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti. 25Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere.

Currently Selected:

2 SAMUELE 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in