YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE 4

4
Isiboseti aphedwa, Davide alanga omupha
1 # Ezr. 4.4; Yes. 13.7 Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Saulo, anamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, manja ake anafooka, ndi Aisraele onse anavutika. 2Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini; 3ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino.
4 # 2Sam. 9.3 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.
5Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana. 6Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa. 7Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse. 8#1Sam. 19.2, 10-11Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Saulo, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera chilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Saulo ndi mbeu yake. 9#Mas. 31.7Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, 10#2Sam. 1.2, 4muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Saulo wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilagi, ndiyo mphotho yake ndinampatsa chifukwa cha uthenga wake. 11#Gen. 9.5-6Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi? 12Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni.

Currently Selected:

2 SAMUELE 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in