2 SAMUELE 3
3
1Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere.
Ana obadwira Davide ku Hebroni
2Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Aminoni, wa Ahinowamu wa ku Yezireele; 3wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; 4ndi wachinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wachisanu Sefatiya mwana wa Abitala; 5ndi wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni.
Abinere apangana ndi Davide
6Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo. 7Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga? 8Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu. 9Mulungu alange Abinere, naonjezepo, ndikapanda kumchitira Davide monga Yehova anamlumbirira; 10kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba. 11Ndipo iye sanakhoze kuyankha Abinere mau amodzi chifukwa cha kumuopa iye. 12Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu. 13#1Sam. 18.20Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga. 14#1Sam. 18.25, 27Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi. 15#1Sam. 25.44Pomwepo Isiboseti anatumiza namchotsera kwa mwamuna wake, kwa Palatiele mwana wa Laisi. 16Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.
17Ndipo Abinere analankhula nao akulu a Israele nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu; 18#2Sam. 3.9chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse. 19#1Mbi. 12.29Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini. 20Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero. 21Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.
Yowabu apha Abinere
22Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere. 23Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere. 24Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi. 25Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu. 26Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe. 27#1Maf. 2.5Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake. 28Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova; 29#1Maf. 2.32-33chilango chigwere pa mutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya. 30Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.
Davide alira Abinere
31 #
Gen. 37.34; 2Sam. 1.2, 11 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha. 32Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse. 33#2Sam. 1.17Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti,
Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?
34Manja anu sanamangidwe,
mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo;
monga munthu wakugwa ndi anthu oipa
momwemo mudagwa inu.
Ndipo anthu onse anamliranso. 35Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa. 36Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse. 37Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumira kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere. 38Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwa kodi kuti kalonga, ndi munthu womveka, wagwa lero m'Israele? 39#Mas. 28.4; 34.16; 2Tim. 4.14Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.
Currently Selected:
2 SAMUELE 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi