2 SAMUELE 2
2
Davide alowa ufumu wa Yuda
1 #
1Sam. 23.2, 4, 9 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni. 2Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. 3Ndipo Davide anakwera nao anyamata ake okhala naye, munthu yense ndi banja lake; iwowa nakhala m'midzi ya Hebroni. 4#1Sam. 31.11, 13; 2Sam. 4.11Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo. 5#Rut. 2.20Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika. 6#2Tim. 1.16, 18Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi. 7Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
Isiboseti alowa ufumu wa Israele
8Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu; 9namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse. 10Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide. 11Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.
Ayuda ndi Aisraele alimbana ku Gibiyoni
12Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni. 13Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. 14Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire. 15Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide. 16Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni. 17Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abinere ndi anthu a Israele anathawa pamaso pa anyamata a Davide. 18Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala. 19Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. 20Pomwepo Abinere anacheuka nati, Kodi ndi iwe Asahele? Iye nayankha, Ndine. 21Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye. 22Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu? 23Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwake, ndi khalilo linatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo. 24Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, pa njira ya ku chipululu cha Gibiyoni. 25Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda. 26Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao? 27Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake. 28Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso. 29Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu. 30Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele. 31Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abinere, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi. 32Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.
Currently Selected:
2 SAMUELE 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi