YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 9

9
Yehu adzozedwa mfumu ya Israele
1Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi. 2#2Maf. 9.5, 11Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo. 3#1Maf. 19.16Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pake, nunene, Atero Yehova, Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israele. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osachedwa, 4Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Giliyadi. 5Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe. 6#1Maf. 19.16Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele. 7#1Maf. 18.4Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele. 8#1Maf. 21.21Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israele. 9#1Maf. 14.10Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya. 10#1Maf. 21.23; 2Maf. 9.35-36Ndipo agalu adzamudya Yezebele pa dera la Yezireele, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa. 11#Yoh. 10.20; Mac. 26.24; 1Ako. 4.10Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake. 12Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine chakutichakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israele. 13#1Maf. 1.34; Mat. 21.7Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.
Yehu awapha Yoramu ndi Ahaziya
14Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu; 15#2Maf. 8.28-29koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezireele ampoletse mabala ake anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kutuluka m'mudzi kukafotokozera m'Yezireele. 16Nayenda Yehu m'galeta, namuka ku Yezireele, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu. 17Ndipo mlonda ali chilili pachilindiro m'Yezireele, naona gulu la Yehu lilinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi? 18Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera. 19Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. 20Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka. 21#1Maf. 21.29; 2Mbi. 22.7Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m'galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezireele. 22Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele? 23Natembenuza Yoramu manja ake, nathawa, nati kwa Ahaziya, Chiwembu, Ahaziya. 24Nafa nao Yehu uta wake, nalasa Yoramu pachikota, nutuluka muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake. 25#1Maf. 21.29Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu. 26#1Maf. 21.19Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova. 27Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko. 28Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide.
29Ndipo pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.
Imfa ya Yezebele
30Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera. 31#1Maf. 16.9-20Ndipo polowa Yehu pachipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimiri, iwe wakupha mbuyako? 32Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu. 33Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi. 34#1Maf. 16.31Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu. 35Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja. 36#1Maf. 21.23Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele; 37#Yer. 8.2ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.

Currently Selected:

2 MAFUMU 9: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in