YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 8

8
Wa ku Sunemu abwera kwao itatha njalayo
1 # 2Maf. 4.35; Mas. 105.16; Hag. 1.11 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri. 2Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri. 3Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. 4#2Maf. 5.27Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita. 5#2Maf. 4.35Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo? 6Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino.
Hazaele mfumu ya Aramu
7Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno. 8#2Maf. 1.2Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m'dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi? 9Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi? 10#2Maf. 8.15Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu. 11Ndipo anamyang'ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu. 12#2Maf. 10.32Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati. 13#1Maf. 19.15Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu. 14Ndipo anachoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wake; ameneyo ananena naye, Anakuuza chiyani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzachira ndithu. 15Ndipo kunali m'mawa mwake, anatenga chimbwi, nachiviika m'madzi, nachiphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaele analowa ufumu m'malo mwake.
Yehoramu mfumu ya Yuda
16Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu. 17Ndiye wa zaka makumi atatu ndi chiwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. 18#2Maf. 8.26Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova. 19#1Maf. 11.36Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza. 20Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha. 21Pamenepo Yoramu anaoloka kunka ku Zairi, ndi magaleta ake onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magaleta, nathawira anthu kwa mahema ao. 22Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi. 23Ndi machitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda. 24Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Ahaziya mfumu ya Yuda
25Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. 26#2Maf. 8.18Ahaziya ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu chaka chimodzi. Ndi dzina la make ndiye Ataliya mdzukulu wa Omuri mfumu ya Israele. 27#2Mbi. 22.3-4Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu. 28Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu. 29Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezireele mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, pakuti anadwala.

Currently Selected:

2 MAFUMU 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in