2 MAFUMU 10
10
Yehu aononga mbumba ya Ahabu
1Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti, 2Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida, 3musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu. 4Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji? 5Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani. 6Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera. 7#1Maf. 21.21Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele. 8Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m'mawa. 9#2Maf. 9.14, 24Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani? 10#1Maf. 21.21, 29Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya. 11Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense. 12Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira, 13Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu. 14Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense.
Aphedwa aneneri a Baala
15 #
Ezr. 10.19; Yer. 35.6-10 Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta. 16Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake. 17#1Maf. 10.7Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya. 18Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri. 19Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala. 20Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira. 21#1Maf. 16.32Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa. 22Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala. 23Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha. 24#1Maf. 20.39Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake. 25Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumudzi wa nyumba ya Baala. 26#1Maf. 14.23Natulutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha. 27Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino. 28Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israele.
Yehu apembedza mafano
29 #
1Maf. 12.28-29
Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala m'Betele ndi m'Dani. 30#2Maf. 10.35; 13.1, 10; 14.23; 15.8Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. 31Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.
32 #
2Maf. 8.12
Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m'malire onse a Israele, 33kuyambira ku Yordani kum'mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani. 34Ndipo machitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazichita, ndi mphambu yake yonse, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 35Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika m'Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. 36Ndipo masiku ake akukhala Yehu mfumu ya Israele m'Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.
Currently Selected:
2 MAFUMU 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi