YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 11

11
1 # 2Maf. 8.26 Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu. 2Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe. 3Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.
4 # 2Mbi. 23 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu. 5#1Mbi. 9.23-25Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu, 6ndi lina lizikhala ku chipata cha Suri, ndi lina ku chipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuitchinjiriza. 7Ndipo magawo awiri a inu, ndiwo onse otulukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu. 8Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m'manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye. 9Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo. 10Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova. 11Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m'manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu. 12#Deut. 17.18-20; 1Sam. 10.24Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo. 13Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova; 14#2Maf. 23.2napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu. 15Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova. 16Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo.
17 # 2Sam. 5.3 Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu. 18#Deut. 12.3Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova. 19Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu. 20Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mudzi munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu. 21#2Mbi. 24.1Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

Currently Selected:

2 MAFUMU 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in