2 MAFUMU 6
6
Elisa ayandamitsa chitsulo pamadzi
1Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu patichepera 2Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani. 3Ndipo wina anati, Mulole mupite nafe anyamata anu. Nati, Ndidzamuka. 4Namuka nao, nafika ku Yordani, iwo natema mitengo. 5Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka. 6#2Maf. 2.21Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo. 7Nati, Katole. Natambasula dzanja lake, naitenga.
Aaramu alangidwa ndi khungu ku Dotana
8Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti. 9Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko. 10Pamenepo mfumu ya Israele inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumchenjeza; nadzisunga osapitako, kawirikawiri. 11Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani? 12Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo. 13#Gen. 37.17Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani. 14Pamenepo anatumizako akavalo ndi magaleta ndi khamu lalikulu, nafikako usiku, nauzinga mudziwo. 15Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji? 16#2Mbi. 32.7-8; Aro. 8.31Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo. 17#2Maf. 2.11; Luk. 24.31Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa. 18#Gen. 19.11Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu uchite khungu. Ndipo Iye anawakantha, nawachititsa khungu, monga mwa mau a Elisa. 19Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? Ngati mudzi ndi uwu? Munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya. 20Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya. 21Niti mfumu ya Israele kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga, ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe? 22#Aro. 12.20Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? Apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao. 23#2Maf. 5.2Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.
Aaramu amangira Samariya misasa
24Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse, nakwera, namangira misasa Samariya. 25Koma m'Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli a siliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu. 26Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu. 27Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa? 28Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa. 29#Deut. 28.53, 57Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wake ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wake. 30#1Maf. 21.27Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zovala zake alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali chiguduli m'kati pa thupi lake. 31#Mas. 34.7; 1Maf. 19.2Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.
Elisa aneneratu za chakudya chochuluka
32 #
Ezk. 8.1
Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake? 33#Yob. 2.9Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?
Currently Selected:
2 MAFUMU 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi