2 MAFUMU 5
5
Naamani wakhateyo achiritsidwa
1 #
Luk. 4.27
Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate. 2Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu. 3Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamchiritsa khate lake. 4Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti. 5#1Sam. 9.8Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi. 6Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake. 7#Gen. 30.2Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine. 8Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israele. 9M'mwemo Naamani anadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa. 10#Yoh. 9.7Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordani kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka. 11Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo. 12Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israele? Ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda. 13Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke? 14#Yob. 33.25; Luk. 4.27Potero anatsika, namira m'Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka. 15#Gen. 33.11; Dan. 6.26Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu. 16#Gen. 14.23; Mat. 10.8; Mac. 8.18, 20Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana. 17Ndipo Naamani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova. 18#2Maf. 7.2, 17Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi. 19Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anachoka, nayenda kanthawi.
Gehazi alangidwa ndi khate
20Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye. 21Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi? 22Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri. 23Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza. 24Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manja mwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nachoka. 25Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse? 26Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi? 27#Num. 12.10; 1Tim. 6.10Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbu ngati chipale chofewa.
Currently Selected:
2 MAFUMU 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi