2 MAFUMU 4
4
Elisa achulukitsa mafuta a mkazi wamasiye
1 #
Lev. 25.39; Mat. 18.25 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake. 2Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta. 3#2Maf. 3.16Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono. 4Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo. 5Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira. 6Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka. 7Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.
Mkazi wa ku Sunemu ndi mwana wake
8 #
1Sam. 25.3; 2Sam. 19.32 Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate. 9Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wake, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano chipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu. 10Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo. 11Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'chipinda chosanja, nagona komweko. 12Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake. 13Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga. 14Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba. 15Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo. 16#Gen. 18.10, 14Ndipo anati, Nyengo yino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu. 17Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye. 18Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anatuluka kunka kwa atate wake, ali kwa omweta tirigu. 19Nati kwa atate wake, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amake. 20Namnyamula, napita naye kwa amake. Ndipo anakhala pa maondo ake kufikira usana, namwalira. 21Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, natuluka, namtsekera. 22Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso. 23Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino. 24Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza. 25Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja; 26uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino. 27Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi. 28Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga? 29#Luk. 10.4; Mac. 19.12Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo. 30Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata. 31#Yoh. 11.11Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo. 32Ndipo pamene Elisa analowa m'nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pake. 33#1Maf. 17.20-21; Mat. 6.6Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova. 34Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda. 35Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake. 36Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunamu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako. 37Iye nalowa, nagwa pa mapazi ake, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wake, natuluka.
Muli imfa m'nkhalimo
38 #
2Maf. 8.1
Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri. 39Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m'funga mwake, nadza, nazichekerachekera m'nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe. 40Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako. 41#2Maf. 2.21; Eks. 15.25Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe chowawa.
Mikate makumi awiri ikwanira anthu ambiri
42 #
1Sam. 9.7; Mat. 14.16-21; 1Ako. 9.11; Agal. 6.6 Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye. 43Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako. 44Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova.
Currently Selected:
2 MAFUMU 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi