1
2 MAFUMU 4:2
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.
Compare
Explore 2 MAFUMU 4:2
2
2 MAFUMU 4:1
Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.
Explore 2 MAFUMU 4:1
3
2 MAFUMU 4:3
Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.
Explore 2 MAFUMU 4:3
4
2 MAFUMU 4:4
Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.
Explore 2 MAFUMU 4:4
5
2 MAFUMU 4:6
Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.
Explore 2 MAFUMU 4:6
6
2 MAFUMU 4:7
Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.
Explore 2 MAFUMU 4:7
7
2 MAFUMU 4:5
Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.
Explore 2 MAFUMU 4:5
8
2 MAFUMU 4:34
Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.
Explore 2 MAFUMU 4:34
Home
Bible
Plans
Videos