2 MAFUMU 16
16
Ahazi mfumu ya Yuda
1Chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. 2Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake; 3#Lev. 18.21; Mas. 106.37-38popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele. 4Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. 5#2Maf. 15.37Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa. 6Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napirikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komwemo kufikira lero lino. 7Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo. 8#2Maf. 12.18Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya. 9Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.
Guwa la nsembe la ku Damasiko
10Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse. 11Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zochokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko. 12Atafika mfumu kuchokera ku Damasiko, anapenya mfumu guwa la nsembelo, nayandikiza mfumu ku guwa la nsembelo, napereka nsembe pomwepo. 13Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere pa guwa la nsembelo. 14Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati pa guwa la nsembe lake ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa la nsembe lake. 15#Eks. 29.39-41Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Pa guwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo. 16Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi. 17#1Maf. 7.23-28; 2Mbi. 28.24Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala. 18Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya. 19Machitidwe ena tsono adawachita Ahazi, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 20Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Hezekiya mwana wake.
Currently Selected:
2 MAFUMU 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi