YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 15

15
Azariya mfumu ya Yuda
1Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. 2Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu. 3Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya. 4#2Maf. 12.3Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. 5#2Mbi. 26.19-23Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko. 6Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 7Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Yotamu mwana wake.
Zekariya mfumu ya Israele
8Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi. 9Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. 10Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake. 11Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. 12#2Maf. 10.30Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.
Salumu mfumu ya Israele
13Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya. 14Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake. 15Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
Menahemu mfumu ya Israele
16Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.
17Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya. 18Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. 19#1Mbi. 5.26Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake. 20Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m'dzikomo. 21Machitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 22Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Pekahiya mwana wake.
Pekahiya mfumu ya Israele
23Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri. 24Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. 25Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake. 26Machitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazichita, taonani zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
27Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri. 28Nachita choipa pamaso pa Yehova, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
Peka mfumu ya Israele
29 # 1Mbi. 5.26 Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya. 30Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya. 31Machitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
Yotamu mfumu ya Yuda
32Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. 33Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki. 34Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya. 35#2Maf. 15.4Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova. 36Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 37#Yes. 7.1Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye. 38Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m'malo mwake Ahazi mwana wake.

Currently Selected:

2 MAFUMU 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in