YouVersion Logo
Search Icon

2 MAFUMU 14

14
Amaziya mfumu ya Yuda ndi Yowasi mfumu ya Israele
1Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. 2Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu. 3Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake. 4Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. 5#2Maf. 12.20Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake; 6#Deut. 24.16koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha. 7Anapha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.
8Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso. 9#Ower. 9.8-15Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo. 10#Deut. 8.14; Ezk. 28.2, 5, 17Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe; 11#2Maf. 23.29Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda. 12Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake. 13Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai. 14#1Maf. 7.51Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya. 15Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 16Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Yerobowamu mwana wake.
17Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu. 18Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 19#2Mbi. 25.27Ndipo anamchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko. 20Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide. 21Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya. 22Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.
Yerobowamu wachiwiri mfumu ya Israele
23Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi. 24Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. 25Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere. 26#2Maf. 13.4Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele. 27#2Maf. 13.5Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yowasi. 28Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 29Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake.

Currently Selected:

2 MAFUMU 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in