2 MAFUMU 13
13
Yoahazi mfumu ya Israele
1Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri. 2Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke. 3#Ower. 2.14Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m'dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo. 4#Eks. 3.7; 2Maf. 14.26; Mas. 78.34Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja. 5#2Maf. 13.25; Neh. 9.27Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale. 6Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; nichitsalanso chifanizo m'Samariya. 7#Amo. 1.3-4Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo. 8Machitidwe ena tsono a Yehowahazi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 9Ndipo Yehowahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'Samariya; nakhala mfumu m'malo mwake Yowasi mwana wake.
Yowasi mfumu ya Israele
10Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi. 11Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo. 12#2Mbi. 25.17-24Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 13Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.
Kumwalira kwa Elisa
14 #
2Maf. 2.12
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! 15Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mivi; nadzitengera uta ndi mivi. 16Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu. 17Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha. 18Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka. 19Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.
20Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m'dziko poyambira chaka. 21Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.
22 #
2Maf. 8.12
Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi. 23#Eks. 32.13Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake. 24Nafa Hazaele mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m'malo mwake Benihadadi mwana wake. 25#2Maf. 13.18-19Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wake ndi nkhondo. Yowasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israele.
Currently Selected:
2 MAFUMU 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi