2 MAFUMU 17
17
Hoseya mfumu yotsiriza ya Israele
1Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai. 2Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye. 3#2Maf. 18.9Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo. 4Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi.
Asiriya apasula Samariya, Aisraele natengedwa ukapolo
5 #
2Maf. 18.9
Pamenepo mfumu ya Asiriya anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu. 6#Lev. 26.32-33; 2Maf. 18.10-11; Hos. 13.16Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi. 7Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina, 8#Lev. 18.3nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza. 9#2Maf. 18.8Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumudzi walinga komwe. 10#Yes. 57.5Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira; 11nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova; 12#Eks. 20.3-4natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musachita ichi. 13#Yer. 18.11; 25.5; 35.5Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri. 14#Deut. 31.27; Miy. 29.1Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao. 15#Deut. 29.25-28Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa. 16#Eks. 32.8; 1Maf. 12.28Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala. 17#1Maf. 21.20; 2Maf. 16.3Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake. 18#1Maf. 11.13, 32Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha. 19#Yer. 3.8Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israele amene adawaika. 20Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake. 21#1Maf. 11.11, 31; 1Maf. 12.20, 28Pakuti anang'amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu. 22Nayenda ana a Israele m'zolakwa zonse za Yerobowamu, zimene anazichita osazileka; 23#2Maf. 17.13mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.
Mfumu ya Asiriya amangitsa alendo m'midzi ya Samariya
24 #
Ezr. 4.2, 10 Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m'midzi mwake. 25Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaope Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa. 26Motero ananena ndi mfumu ya Asiriya, kuti, Amitundu aja mudawachotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; chifukwa chake anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, ilikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli. 27Pamenepo mfumu ya Asiriya analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawachotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli. 28Nadza wina wa ansembewo adawachotsa ku Samariya, nakhala ku Betele, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova. 29Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uliwonse m'midzi mwao mokhala iwo. 30#2Maf. 17.24Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima, 31#Lev. 18.21ndi Aavi anapanga Nibihazi ndi Taritaki; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. 32#1Maf. 12.31Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje. 33#Zef. 1.5; Mat. 6.24Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako. 34Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele, 35#Ower. 6.10ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu ina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe; 36#Eks. 6.6; Deut. 10.20koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe; 37#Deut. 5.32ndi malemba, ndi maweruzo, ndi chilamulo, ndi choikika anakulemberani muzisamalira kuzichita masiku onse, nimusamaopa milungu ina; 38ndi chipangano ndinachichita nanu musamachiiwala, kapena kuopa milungu ina iai; 39koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse. 40Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba. 41#2Maf. 17.32-33Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.
Currently Selected:
2 MAFUMU 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi