YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 29

29
Hezekiya mfumu ya Yuda
1 # 2Maf. 18.1-3 Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya. 2Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adachitira Davide kholo lake. 3#2Mbi. 28.24Chaka choyamba cha ufumu wake, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso. 4Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamaso poyera kum'mawa, 5#1Mbi. 15.12nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m'malo opatulika. 6#Yer. 2.27Pakuti analakwa makolo athu, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya chokhalamo Yehova, namfulatira. 7#2Mbi. 28.24Anatsekanso pa khomo chipinda cholowera, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israele. 8#2Mbi. 24.18Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale chodabwitsa ndi chotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu. 9#2Mbi. 28.5-6, 8, 17Pakuti taonani, makolo athu adagwa ndi lupanga, ndi ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali andende chifukwa cha ichi. 10#2Mbi. 15.12Tsono mumtima mwanga nditi ndichite chipangano ndi Yehova Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kutichokera. 11#Num. 8.14Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.
Alevi ayeretsa Kachisi
12Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yowele mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; ndi a Ageresoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa; 13ndi a ana a Elizafani, Simiri ndi Yeuwele; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya; 14ndi a ana a Hemani, Yehuwele ndi Simei; ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyele. 15#2Mbi. 29.5Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova. 16Ndipo ansembe analowa m'kati mwake mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, natulutsira kubwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kachisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuzitulutsira kunja kumtsinje wa Kidroni. 17Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira kuchipinda cholowera cha nyumba ya Yehova tsiku lachisanu ndi chitatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi. 18Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zake zonse. 19#2Mbi. 28.24Zipangizo zonse zomwe adazitaya mfumu Ahazi m'ufumu wake m'kulakwa kwake kuja, tazikonza, ndi kuzipatula; ndipo taonani, zili kuguwa la nsembe la Yehova.
Hezekiya aikanso chipembedzo cha Yehova
20Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mudzi, nakwera kunka kunyumba ya Yehova. 21#Lev. 4.14Ndipo anabwera nazo ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi anaankhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yauchimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova. 22#Lev. 8.14-15, 19; Aheb. 9.21-22Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso anaankhosa aja, nawaza mwazi pa guwa la nsembe. 23Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yauchimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao, 24#Lev. 4.13-21ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse. 25#1Mbi. 16.4-6Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake. 26Alevi tsono anaimirira ndi zoimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga. 27#2Mbi. 23.18Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoimbira za Davideyo mfumu ya Israele. 28Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza. 29#2Mbi. 20.18Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira. 30Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira. 31Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza. 32Ndi kuwerenga kwake kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi anaankhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova. 33Ndi zinthu zopatulika zinafikira ng'ombe mazana asanu ndi limodzi, ndi nkhosa zikwi zitatu. 34#2Mbi. 30.3Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula. 35#Lev. 3.16Ndiponso zidachuluka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iliyonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka. 36Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ichi Mulungu adakonzeratu; pakuti chinthuchi chidachitika modzidzimutsa.

Currently Selected:

2 MBIRI 29: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in