YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 28

28
Ahazi mfumu yoipitsitsa ya Yuda
1 # 2Maf. 16.2-4 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake, 2#Eks. 34.17koma anayenda m'njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaala mafano oyenga. 3Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele. 4Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. 5#Yes. 7.1Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe akulu. 6#2Maf. 15.27Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. 7Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu. 8Ndipo ana a Israele anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana aamuna ndi aakazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya. 9Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba. 10#Lev. 25.39, 43Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu? 11#Yak. 2.13Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu. 12Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo, 13nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele. 14Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga msonkhano wonse. 15#2Maf. 6.22; Miy. 25.21-22; Luk. 6.27; Aro. 12.20Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.
16 # 2Maf. 16.7-9 Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize. 17Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende. 18#Ezk. 16.27-28, 57Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi milaga yake, ndi Timna ndi milaga yake, ndi Gimizo ndi milaga yake; nakhala iwo komweko. 19Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri. 20Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa. 21Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo. 22Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo. 23#2Mbi. 25.14; Yer. 44.17-18Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse. 24#2Maf. 16.17Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngodya zilizonse za Yerusalemu. 25Ndi m'midzi iliyonse ya Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake. 26Machitidwe ena tsono, ndi njira zake zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. 27Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

Currently Selected:

2 MBIRI 28: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in