2 MBIRI 27
27
Yotamu mfumu ya Yuda
1 #
2Maf. 15.32-38
Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki. 2Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe m'Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda. 3Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu. 4Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe. 5Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe. 6Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake. 7Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda. 8Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi. 9Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Currently Selected:
2 MBIRI 27: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi