YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 30

30
Hezekiya achita Paska ku Yerusalemu
1Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska. 2Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa m'Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri. 3#2Mbi. 29.34Pakuti sanakhoze kumchita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikire, ndi anthu sadasonkhane ku Yerusalemu. 4Ndipo chinthuchi chinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse. 5Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikulu sanachite monga mudalembedwa. 6#Yer. 4.1; Yow. 2.12-13Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asiriya. 7#Ezk. 20.18Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene analakwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya. 8#2Maf. 17.14Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu. 9#Eks. 34.6-7; Yes. 55.7Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye. 10Ndipo amtokoma anapitira m'midzi yonse ya dziko la Efuremu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola. 11#2Mbi. 15.9; 30.18, 21Komatu ena a Asere ndi Manase ndi a Zebuloni anadzichepetsa, nadza ku Yerusalemu. 12#Afi. 2.13Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova. 13Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa mwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu. 14#2Maf. 23.6Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kidroni. 15#2Mbi. 29.34Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova. 16Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa chilamulo cha Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira kudzanja la Alevi. 17Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatule; potero Alevi anayang'anira kupha za Paska kwa aliyense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova. 18#2Mbi. 30.11Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense 19#2Mbi. 19.3wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika. 20Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawachiritsa anthu. 21Ndipo ana a Israele opezeka m'Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova. 22Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao. 23#1Maf. 8.65Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe. 24#2Mbi. 30.15Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula. 25#2Mbi. 30.18Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala m'Yuda, anakondwera. 26Momwemo munali chimwemwe chachikulu m'Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitika chotero m'Yerusalemu. 27#Num. 6.23-27; Deut. 26.15Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.

Currently Selected:

2 MBIRI 30: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in