1 SAMUELE 31
31
Saulo ndi ana ake atatu aphedwa ndi Afilisti pa Gilibowa
1 #
1Mbi. 10.1-12
Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. 2Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo. 3#2Sam. 1.6-10Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo. 4Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera. 5Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye. 6Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija. 7Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo. 8Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa. 9Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu. 10Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani. 11Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo, 12#2Sam. 2.4-7; 2Mbi. 16.14ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko. 13#Gen. 50.10; 2Sam. 21.12-14Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli m'Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.
Currently Selected:
1 SAMUELE 31: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi