YouVersion Logo
Search Icon

2 SAMUELE Mau Oyamba

Mau Oyamba
Bukuli likukamba za ufumu wa Davide ndiponso za nkhondo zimene iye anamenya ndi adani ake m'dziko mwake ndiponso ndi maiko oyandikana ndi dziko la Israele, pofuna kulimbitsa ndi kukulitsa ufumu wakewo.
Davide anali munthu wa chikhulupiriro cholimba ndi wokonda Mulungu kwambiri, ndipo amadziwa kukopa mitima ya anthu ake. Komabe nthawi zina anagwa m'machimo oopsa chifukwa chotsata zilakolako ndi zikhumbitso zoipa. Mneneri Natani atamdzudzula chifukwa cha zoipazo, iye anadzichepetsa navomera kuti walakwadi nkuvomera chilango chimene Mulungu apereka.
Aisraele adatengeka mtima ndi mfumu Davide, ndipo patapita zaka zambiri, pamene dziko lao lidapasuka, Aisraelewo ankakumbukira khalidwe lake abwino ndi ntchito zake zazikulu, kotero kuti ankalakalaka kukhalanso ndi mfumu ina yokhala ndi mtima ngati wa Davide, pakati pa zidzukulu zake.
Za mkatimu
Ufumu wa Davide mu dziko la Yuda 1.1—4.12
Ufumu wa Davide m'dziko lonse la Israele 5.1—24.25
a. Zaka zoyamba 5.1—10.19
b. Davide ndi Bateseba 11.1—12.25
c. Ana ake amuukira ndiponso zovuta zina 12.26—20.26
d. Zaka zotsiriza za ufumu wake 21.1—24.25

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in