YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 30

30
Davide alanditsa a ku Zikilagi m'manja mwa Aamaleke
1 # 1Sam. 27.6 Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto; 2nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akulu ndi ang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka. 3Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo. 4Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso. 5Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. 6#Eks. 17.4; Mas. 42.5-6; Hab. 3.17-18Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.
7 # 1Sam. 23.6, 9 Ndipo Davide ananena ndi Abiyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abiyatara nabwera ndi efodi kwa Davide. 8#1Sam. 23.2, 4Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse. 9Chomwecho Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena. 10#1Sam. 30.21Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori. 11Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa; 12nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi. 13Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu. 14Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto. 15Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene. 16Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda. 17Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa. 18Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleke, napulumutsa akazi ake awiri. 19#1Sam. 30.8Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana amuna kapena ana akazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse. 20Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide. 21#1Sam. 30.10Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji. 22Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke. 23Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe. 24#Num. 31.27; Yos. 22.8Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi. 25Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele.
26Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova. 27Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri; 28ndi kwa iwo a ku Aroere, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Esitemowa; 29ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m'midzi ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m'midzi ya Akeni; 30ndi kwa iwo a ku Horoma, ndi kwa iwo a ku Borasani, ndi kwa iwo a ku Ataki; 31ndi kwa iwo a ku Hebroni, ndi kumalo konse kumene Davide ndi anthu ake ankayendayenda.

Currently Selected:

1 SAMUELE 30: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in