1 SAMUELE 3
3
Masomphenya a Samuele
1 #
1Sam. 2.11, 18; Amo. 8.11 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke. 2Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino); 3#Lev. 24.2-3ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona m'Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu. 4Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano. 5Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitana, kagone. Napita iye, nagona. 6Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone. 7#1Ako. 3.1Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye. 8Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo. 9Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake. 10Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva. 11#2Maf. 21.12; Yer. 19.3Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva. 12Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza. 13#1Sam. 2.12, 17, 22-25; Ezk. 7.3Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse. 14#Yes. 22.14Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.
Samuele awulula kwa Eli
15Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo. 16Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine. 17Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe. 18#Yob. 2.10Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.
19 #
Gen. 39.2; 1Sam. 9.6 Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe. 20Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova. 21Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.
Currently Selected:
1 SAMUELE 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi