YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 4

4
Afilisti akantha Aisraele
1 # 1Sam. 7.12 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki. 2Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.
Likasa lilandidwa, Hofeni ndi Finehasi aphedwa
3Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu. 4#Eks. 25.18, 22Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Yehova. 5Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi. 6Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo. 7Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza kale lonse panalibe chinthu chotere. 8Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi. 9#1Ako. 16.13Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. 10#1Sam. 4.2Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi. 11#1Sam. 2.32, 34; Mas. 78.61Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa. 12#2Sam. 1.2; Yos. 7.6; Neh. 9.1Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Imfa ya Eli
13Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira. 14Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli. 15Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya. 16#2Sam. 1.4Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga? 17Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa. 18Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai. 19Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera. 20Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira. 21Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake. 22Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.

Currently Selected:

1 SAMUELE 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for 1 SAMUELE 4