1 SAMUELE 2
2
Choyamikira cha Hana
1 #
Luk. 1.46-55
Ndipo Hana anapemphera, nati,
Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova,
nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova;
pakamwa panga pakula kwa adani anga;
popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.
2 #
Eks. 15.11
Palibe wina woyera ngati Yehova;
palibe wina koma Inu nokha;
palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.
3Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero;
m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa;
chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru,
ndipo Iye ayesa zochita anthu.
4Mauta a amphamvu anathyoka,
koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'chuuno.
5Amene anakhuta anakasuma chakudya;
koma anjalawo anachira;
inde chumba chabala asanu ndi awiri;
ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.
6 #
Deut. 32.39
Yehova amapha, napatsa moyo;
Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.
7 #
Yob. 1.21
Yehova asaukitsa, nalemeza;
achepetsa, nakuzanso.
8 #
Mas. 113.7-8
Amuutsa waumphawi m'fumbi,
nanyamula wosowa padzala,
kukamkhalitsa kwa akalonga;
ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero.
Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,
ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.
9 #
Mas. 121.3
Adzasunga mapazi a okondedwa ake,
koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima;
pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.
10 #
Mas. 96.10, 13 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;
kumwamba Iye adzagunda pa iwo;
Yehova adzaweruza malekezero a dziko.
Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake,
nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.
11Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.
Kuchimwa kwa ana a Eli
12 #
Ower. 2.10; Aro. 1.28 Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova. 13Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; 14nachipisa m'chimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko. 15#Lev. 3.3-16Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi. 16Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda. 17#Mala. 2.8Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova. 18Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta. 19#1Sam. 1.3Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka. 20#1Sam. 1.28Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao. 21#Ower. 13.24; Luk. 2.40Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.
22 #
Eks. 38.8
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako. 23Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa. 24Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova. 25#Num. 15.30; Deut. 32.35; Yos. 11.20Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga. 26#Luk. 2.52; Aro. 14.18Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.
Mneneri aneneratu za kupasuka kwa banja la Eli
27Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Ejipito, m'nyumba ya Farao? 28#Eks. 28.1, 4; Lev. 2.3, 10Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? 29#1Sam. 3.13Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga? 30#Yer. 18.9Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa. 31#1Maf. 2.27Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba, 32Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire. 33Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri. 34#1Sam. 4.11Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri. 35Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse. 36Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.
Currently Selected:
1 SAMUELE 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi