YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 15

15
Abiya atsata zoipa za atate wake Rehobowamu
1Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda. 2Anakhala mfumu zaka zitatu m'Yerusalemu, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu. 3#1Maf. 11.4Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake. 4#1Maf. 11.36Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu; 5#2Sam. 11.4-27chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti. 6Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wake. 7#2Mbi. 13.2-3, 22Ndipo machitidwe ake ena a Abiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu. 8Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m'malo mwake.
Maweruzidwe okoma a Asa
9Ndipo chaka cha makumi awiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda. 10Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu chimodzi, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu. 11Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake. 12#1Maf. 22.46Nachotsa m'dziko anyamata aja adama, nachotsanso mafano onse anawapanga atate ake. 13#2Mbi. 15.16Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni. 14Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse. 15Ndipo analonga m'nyumba ya Yehova zinthu zija atate wake adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasiliva ndi zagolide ndi zotengera.
Nkhondo ya pakati pa Asa ndi Baasa
16Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse. 17#2Mbi. 16.1-6Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda. 18Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati, 19#2Mbi. 16.7Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere. 20Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumidzi ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali. 21Tsono Baasa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza. 22#2Mbi. 16.6Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Baasa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa. 23Ndipo machitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yake yonse, ndi zonse anazichita, ndi midzi anaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wake anadwala mapazi ake. 24Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.
Baasa akantha mbumba ya Yerobowamu nakhala mfumu ya Israele
25Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. 26#1Maf. 14.16Nachita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi m'tchimo lomwelo iye akachimwitsa nalo Aisraele. 27Ndipo Baasa mwana wa Ahiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira chiwembu; ndipo Baasa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisraele onse adamangira misasa Gibetoni. 28Inde Baasa anamupha chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake. 29#1Maf. 14.9-16Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo; 30chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele. 31Ndipo machitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 32Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.
33Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai. 34#1Maf. 15.26Ndipo anachimwa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake iye anachimwitsa nalo Israele.

Currently Selected:

1 MAFUMU 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in