1 MAFUMU 16
16
Yehu aneneratu kugwa kwa Baasa
1Ndipo mau a Yehova akutsutsa Baasa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati, 2#1Maf. 15.34Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao; 3taona, ndidzachotsa psiti Baasa ndi nyumba yake, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, 4#1Maf. 14.11Agalu adzadya aliyense wa Baasa amene adzafera m'mudzi, ndipo amene adzafera m'thengo zidzamudya mbalame za m'mlengalenga. 5#2Mbi. 16.11Tsono machitidwe ena a Baasa, ndi ntchito zake, ndi mphamvu zake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 6Nagona Baasa ndi makolo ake, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wake analowa ufumu m'malo mwake. 7Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.
Ela, Zimri, ndi Omuri, mafumu a Israele
8Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri. 9Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang'anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza. 10Nalowamo Zimiri, namkantha, namupha chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri za Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake. 11Ndipo kunali, atalowa ufumu wake, nakhala pa mpando wachifumu wake, anawakantha onse a m'nyumba ya Baasa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ake, kapena wa mabwenzi ake. 12#1Maf. 16.3Motero Zimiri anaononga nyumba yonse ya Baasa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Baasa, mwa dzanja la Yehu mneneri, 13chifukwa cha machimo onse a Baasa, ndi machimo a Ela mwana wake anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao. 14Tsono machitidwe ena a Ela, ndi ntchito zake zonse, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
15Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti. 16Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimiri wachita chiwembu, nakanthanso mfumu; chifukwa chake tsiku lomwelo Aisraele onse a kumisasa anamlonga Omuri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israele. 17Ndipo Omuri anachoka ku Gibetoni, ndi Aisraele onse naye, nakamangira misasa Tiriza. 18Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mudzi, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa; 19#1Maf. 12.28chifukwa cha machimo ake anachimwawo, pakuchita choipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake anachimwa nalolo, nachimwitsa nalo Aisraele. 20Machitidwe ena tsono a Zimiri, ndi chiwembu anachichitacho, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
21Pamenepo anthu a Israele anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omuri. 22Koma anthu akutsata Omuri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omuri nakhala mfumu. 23Chaka cha makumi atatu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anayamba kukhala mfumu ya Israele, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi chimodzi. 24Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri a siliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mudzi anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho. 25#Mik. 6.16Koma Omuri anachimwa pamaso pa Yehova, nachita zoipa koposa onse adamtsogolerawo. 26Nayenda m'njira yonse ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao. 27Ndipo machitidwe ena a Omuri anawachita, ndi mphamvu yake anaionetsa, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? 28Nagona Omuri ndi makolo ake, naikidwa m'Samariya; ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.
Ahabu mfumu yoipa ya Israele
29Ndipo chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omuri analowa ufumu wa Israele, nakhala Ahabu mwana wa Omuri mfumu ya Israele m'Samariya zaka makumi awiri mphambu ziwiri. 30#1Maf. 16.25; 21.25Ndipo Ahabu mwana wa Omuri anachimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo. 31#Deut. 7.3-4Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira. 32#2Maf. 10.21, 26-27Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga m'Samariya. 33#1Maf. 16.30Ahabu anapanganso chifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israele adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele. 34#Yos. 6.26M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.
Currently Selected:
1 MAFUMU 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi