YouVersion Logo
Search Icon

1 YOHANE 3

3
Ife ndife ana a Mulungu
1 # Yoh. 1.12; 15.18-19 Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye. 2#Yes. 56.5; Aro. 8.18, 29; 1Ako. 13.12Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali. 3#2Ako. 7.1Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. 4Yense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndilo kusaweruzika. 5#1Pet. 2.22Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo. 6#1Yoh. 2.4Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuona Iye, ndipo sanamdziwa Iye. 7#Aro. 2.13Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama: 8#Gen. 3.15; Yoh. 8.44iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi. 9#1Yoh. 5.18; 1Pet. 1.23Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu. 10#1Yoh. 2.29; 4.8M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. 11#Yoh. 13.34Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: 12#Gen. 4.4, 8osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.
13 # Yoh. 15.18-19 Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi. 14#1Yoh. 2.9-11Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa. 15#Agal. 5.21Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye. 16#Yoh. 3.16; 15.13Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale. 17#Luk. 3.11Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? 18#Aro. 12.9Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi. 19#Yoh. 18.37Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m'choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, 20#1Ako. 4.4m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse. 21#Aheb. 10.22Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu; 22#Mas. 34.15; Mat. 7.8ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake. 23#Mat. 22.39; Yoh. 6.29Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira. 24#Yoh. 14.23; 1Yoh. 4.13Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

Currently Selected:

1 YOHANE 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in