1 YOHANE 2
2
1 #
Aro. 8.34
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama; 2#Yoh. 1.29; Aro. 3.25ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.
Za kusunga malamulo, kukondana, ndi kudzimana zapadziko
3Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. 4#1Yoh. 1.6Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi; 5#Yoh. 14.21, 23; 1Yoh. 4.12-13koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye; 6#Yoh. 13.15iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.
7 #
1Yoh. 2.24
Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva. 8#Yoh. 1.9; 8.12; 13.34; Aef. 5.8Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala. 9#1Yoh. 3.14Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino. 10#1Yoh. 3.14Iye amene akonda mbale wake akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11#Yoh. 12.35Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.
12 #
Luk. 24.47
Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake. 13#1Yoh. 1.1Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate. 14#Aef. 6.10Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo. 15#Aro. 12.2; Yak. 4.4Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. 16Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. 17#Yak. 4.14Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
Za okana Khristu
18 #
Mat. 24.5, 24; 2Ate. 2.3 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi. 19#Yoh. 10.28-29; Mac. 20.30; 1Ako. 11.19Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife. 20#Yoh. 14.26; 2Ako. 11.9Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse. 21Sindinakulemberani chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi. 22#1Yoh. 4.3Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana. 23#Yoh. 15.23Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso. 24#Yoh. 14.23Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate. 25#Yoh. 17.2-3Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha. 26Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu. 27#Yoh. 14.26; 1Yoh. 2.20Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye. 28#1Yoh. 3.2Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake. 29#1Yoh. 3.7, 10Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.
Currently Selected:
1 YOHANE 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi