1 YOHANE 1
1
Mau a moyo aoneka m'thupi
1 #
Luk. 24.39; Yoh. 1.1, 14 Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo, 2#Yoh. 1.1-2; 21.24(ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo tichita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife); 3#Mac. 4.20chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu; 4#Yoh. 15.11ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe.
Mulungu ali kuunika; wosayenda m'kuunika alibe chiyanjano ndi Iye
5 #
Yoh. 1.9; 8.12 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima. 6#2Ako. 6.14Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi; 7#Aheb. 9.14koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
Za kuwulula machimo ndi kukhululukidwa
8 #
1Maf. 8.46; Yak. 3.2 Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi. 9#Mas. 32.5; 51.2Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse. 10Tikanena kuti sitidachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife.
Currently Selected:
1 YOHANE 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi